الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.oh inu anthu okhulupirira! Kwaniritsani mapangano anu. Ndi zololedwa kwa inu kudya nyama zonse kupatula zimene tsopano zili kuletsedwa kwa inu. Kusaka nyama ndi koletsedwa pamene muli paulendo wa Hajji. Ndithudi Mulungu amalamula zimene Iye afuna
2.oh inu anthu okhulupirira! Musaphwanye kupatulika kwa zizindikiro za Mulungukapenaza MweziWoyera kapenazanyamazimene zimabweretsedwa kukhala nsembe kapena zizindikiro zimene zimaikidwa pa izo kapena za anthu amene amadza ku Nyumba Yoyera kudzafuna chisomo ndi chisangalalo cha Ambuye wawo. Koma mukatsiriza miyambo ya Hajji, mukhoza kusaka ndipo musalole chidani cha anthu ena amene anakuletsani kulowa mu Mzikiti Woyera kuti chikuchimwitseni. Thandizanani wina ndi mnzake pa ntchito zabwino koma musathandizane mu ntchito ya uchimo ndi yoswa malamulo. Muopeni Mulungu. Ndithudi Mulungu amalanga kwambiri
3.Zoletsedwa kwa inu kudya ndi nyama yofa yokha, liwende, nyama ya nkhumba ndi nyama iliyonse imene yaphedwa m’dzina la mulungu wina osati Mulungu weniweni. Inu muli kuletsedwa kudya nyama zophedwa pomangirira chingwe pakhosi ndi kukoka ndiponso izo zimene zamenyedwa mpaka kufa, nyama zimene zaphedwa chifukwa chakugwa kapena yaphedwa ndi nyama inzake ndiponso imene yadyedwa ndi chilombo cha m’thengo, kupatula ngati inu mwaimaliza kupha ndiponso nyama zimene zaphedwa pamwala ndi kuperekedwa ku milungu ya mafano. Inu mwaletsedwa kufuna kudziwa chinsinsi pochita mayere a maula. Amenewa ndi machitidwe oipa . Lero anthu osakhulupirira achita mantha ndi chipembedzo chanu. Motero musawaope iwo koma opani Ine. Lero ndakonza chipembedzo chanu ndipo ndamaliza ubwino wanga pa inu ndipo Ine ndakusankhirani Chisilamu kuti chikhale chipembedzo chanu. Koma iye amene wakakamizidwa ndi njala osati ndi cholinga chochimwa, ndithudi, Mulungu ali wokhululukira ndi wachisoni
5.Zinthu zonse zabwino, tsiku lalero, zaloledwa kuti mukhoza kuzigwiritsa ntchito. Chakudya cha anthu m’Buku ndi chololedwa kwa inu ndiponso chakudya chanu ndi chololedwa kwa iwo. Muloledwa kukwatira akazi okhulupirira ndi akazi angwiro kuchokera ku gulu la anthu a m’Buku pamene muwapatsa mphatso yawo ya ukwati ndi kukhala molemekezeka ndi iwo osachita chiwerewere kapena kuwasandutsa iwo ngati zibwenzi zanu. Ndipo aliyense amene sakhulupirira mwa Mulungu mmodzi, ntchito zake zidzakhala zopanda pake ndipo m’dziko limene lili nkudza, iye adzakhala olephera kwambiri
6.Oh inu anthu okhulupirira! Pamene mukonzeka kuti mupemphere, sambitsani nkhope zanu ndiponso manja anu mpaka pa kasukusuku ndipo pakani ku mutu kwanu ndipo sambitsani mapazi anu mpaka molekezera phazi lanu. Ngati mwadetsedwa, dziyeretseni. Koma ngati muli kudwala kapena muli paulendo, kapena wina wa inu abwera kuchokera ku chimbudzi kapena munagona ndi akazi anu ndipo mwasowa madzi, tengani mchenga woyera ndi kupukuta m’manja mwanu ndi ku nkhope kwanu. Mulungu safuna kukukundikirani mtolo wolemera koma Iye afuna kukuyeretsani ndi kukwaniritsa zokoma zake kwa inu kuti inu mukhale oyamika
12.Ndithudi Mulungu adalandira lonjezo la ana a Israyeli ndipo Ife tidadzutsa pakati pawo atsogoleri khumi ndi awiri. Ndipo Mulungu adati: “Ine, ndithudi, ndili pamodzi ndi inu ngati inu mupemphera moyenera, mupereka chopereka chothandiza anthu osauka ndipo mukhulupirira mwa Atumwi anga ndipo muwathandiza ndiponso mukongoza Mulungu ngongole yabwino. Ndithudi Ine ndidzakukhululukirani machimo anu ndi kukulowetsani ku minda yothiriridwa ndi madzi ya m’mitsinje. Koma ngati wina wa inu, pambuyo pake sakhulupilira, Iye wasochera ku njira yoyenera.”
41.oh iwe Mtumwi! Asakudandaulitse anthu amene amafulumira kusakhulupirira ndipo amati: “Tikhulupirira” ndi milomo yawo pamene mitima yawo ilibe chikhulupiriro. Ndipo pakati pa Ayuda pali anthu amene amamvetsera mabodza ndi zimene anthu ena amene sadadze kwa iwe amakamba. Iwo amasintha mawu monga momwe adalili ndipo amati: “Ngati mwapatsidwa izi landirani ndipo ngati simudapatsidwe chenjerani.” Ndipo amene Mulungu afuna kumusocheretsa,iwe ulibe mphamvu ina iliyonse pa iye yopikisana ndi Mulungu. Awo ndi amene mitima yawo Mulungu safuna kuiyeretsa ndipo kwa awa kuli zinthu zochititsa manyazi m’dziko lino ndi chilango chachikulu m’dziko limene lili nkudza
48.Ndipo kwa iwe, tavumbulutsa Buku mwachoonadi kutsimikiza Mabuku amene adadza kale, okhulupilika ndi a pamwamba. Kotero weruza pakati pawo ndi zimene wavumbulutsa Mulungu ndipo usatsatire zilakolako zawo kusiya choonadi chimene chavumbulutsidwa kwa iwe. Ife takhazikitsa lamulo ndipo takonza njira yoyenera. Ngati Mulungu akadafuna, akadakupangani inu kukhala mtundu umodzi wa anthu koma afuna kuti akuyeseni inu ndi zimene wakupatsani. Motero pikisanani pochita ntchito zabwino. Ndi kwa Mulungu kumene nonsenu mudzabwerera ndipo Iye adzakuuzani zonse zimene munali kutsutsana
64.Ayudaamanenakuti:“Manjaa Mulungundiomangika.” Manja awo ndiwo akhale omangika ndiponso iwo atembereredwe chifukwa cha zimene anena! Iyayi! Manja onse a Mulungu ndi otambasuka. Iye amapereka mmene wafunira. Ndithudi chimene Mulungu wavumbulutsa kwa iwe chimaonjezera udani ndi kusakhulupirira kwa anthu ambiri mwaiwo. Ife taika pakati pawo ndi kukhazikitsa udani mpaka patsiku louka kwa akufa. Nthawi zonse pamene iwo ayatsa moto wa nkhondo, Mulungu amauzima ndipo iwo amayesetsa kupanga zoipa padziko. Mulungu sakonda anthu oyambitsa chisokonezo
89.Mulungu sadzakulangani inu chifukwa cha kulumbira kwanu kosakonzekera. Koma Iye adzakulangani chifukwa cha malonjezo anu a bodza. Kulipira kwake ndi kudyetsa anthu khumi osowa ndi chakudya chimene inu mumadyetsa banja lanu kapena kuwaveka kapena kumasula kapolo mmodzi. Koma yense amene sangathe kukwaniritsa china cha izi, ayenera kusala masiku atatu. Kumeneko ndiko kulipira kwa malonjezo anu ngati mwalumbira. Motero sungani malonjezo anu. Mmenemo ndimo mmene Mulungu amaonetsera poyera chivumbulutso chake kuti mukhale oyamika
95.Oh inu anthu okhulupirira! Musaphe nyama za m’thengo pamene mutavala zobvala za Hajji kapena Umra. Yense wa inu amene apha nyama mwadala, adzapereka, ngati dipo lofika ku Kaaba, nyama yoweta yofanana ndi imene iye wapha, imene idzatsimikizidwa ndi anthu awiri olungama amene ali pakati panu kapena m’malo mwake adzadyetsa anthu osauka kapena kusala kuti alawe kuipa kwa ntchito zake. Mulungu wakhululukira zonse za m’mbuyo koma ngati wina abwerera ku uchimo, Mulungu adzamulanga kwambiri. Mulungu ndi wamphamvu ndipo ndi mwini kubwezera
106.O inu anthu okhulupirira! Pamene imfa idza pa mmodzi wa inu panthawi yopereka mawu, anthu awiri olungama achitire umboni pakati panu; kapena anthu amuna awiri ochokera kumtundu wina osakhulupirira ngati muli paulendo padziko ndipo imfa yakupezani. Asungeni mpaka mutatha kupemphera ndipo ngati mukaika za kukhulupirika kwawo, afunseni kuti alumbire pali Mulungu kuti: “Ife sitigulitsa umboni wathu pamtengo wina uliwonse ngakhale kwa m’bale wathu weniweni. Ndipo ife sitibisa umboni wa Mulungu, ndithudi ife titatero tikhala mgulu la anthu ochimwa.”
110.Pamene Mulungu adzati: “Oh! iwe Yesu, mwana wamwamuna wa Maria! Kumbukira zokoma zanga zimene ndinakhazikitsa pa iwe ndi pa amayi ako; mmene ndidakulimbitsa iwe ndi Mzimu Woyera moti udalankhula kwa anthu pamene unali wakhanda ndiponso utakula msinkhu; mmene ndidakuphunzitsira iwe mawu a Mulungu ndi kukuonjezera luntha labuku la chipangano chakale ndi chipangano chatsopano; mmene ndi chilolezo changa udapanga kuchokera kudothi, chinthu cholingana ndi mbalame ndipo udachiuzira mpweya ndipo ndi chilolezo changa, icho chidasanduka mbalame ya moyo; ndipo mmene ndi chilolezo changa udachiritsa anthu a khungu ndi anthu a makate ndiponso ndi chilolezo changa unali kupereka moyo kwa anthu akufa; mmene ndidakutetezera iwe kwa ana a Israyeli pamene udadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka,” ndipo anthu osakhulupirira amene adali pakati pawo adati: “Ichi sichina chilichonse koma matsenga oonekera poyera.”