7.Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo, ngati inu nonse mutakhala ndi chikhulupiriro chenicheni
8.Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Ndipo ndiye amene amapereka moyo ndi imfa. Ambuye wako ndi Ambuye wa makolo ako amene adanka kale
17.Ndipo, ndithudi, tidawayesa anthu a Farawo, iwo asanabadwe, ndipo kudadza kwa iwo Mtumwi wolemekezeka
37.Kodi awa ndi opambana kuposa anthu a Tubba ndi iwo amene adalipo kale? Ife tidawaononga onse ndipo iwo adali olakwa
42.Kupatula yekhawo amene waonetsedwa chisomo cha Mulungu. Ndithudi Iye ndiye Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni chosatha
56.Ndipo iwo sadzalawa imfa kupatula imfa yoyamba ndipo Iye adzawapulumutsa ku chilango chowawa cha Gahena
58.Ndithudi Ife taipanga Koraniyi kukhala yapafupi m’chiyankhulo chako ndi cholinga chakuti mwina angathe kukumbukira