3.Motero Mulungu, Mwini mphamvu ndi Mwini nzeru amatumiza chivumbulutso kwa iwe monga anali kuvumbulutsira kwa iwo amene adalipo iwe usanabadwe
4.Iye ndiye Mwini wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndipo Iye ndi wapamwamba, ndiponso wamkulu
5.Kumwamba kumafuna kuphulika chifukwa cha ulemerero wake ndipo angelo amaimba mayamiko a Ambuye wawo ndipo amapempha chikhululukiro cha zolengedwa zonse za padziko lapansi. Ndithudi, Mulungu, ndiye amene amakhululukira ndipo ndi Mwini chisoni chosatha
6.Ndipo iwo amene amasankha ena ake kukhala atetezi awo m’malo mwake, Mulungu amawayang’anira ndipo iwe ulibe ulamuliro pa iwo
7.Kotero tavumbulutsa kwa iwe Buku la Korani m’Chiarabu, kuti ukhoza kuchenjeza make wa Mizinda ndi iyo youzungulira. Ndipo kuti uchenjeze za tsiku la chiweruzo limene mosakayika lidzadza pamene gulu lina lidzakhala ku Paradiso ndi gulu linzake lidzakhala kumoto
8.Ndipo ngati Mulungu akadafuna, akadawapanga onse kukhala mtundu umodzi koma Iye amasankha amene wamufuna kulandira chisomo chake ndipo onse osalungama sadzapeza mtetezi kapena wowathandiza
9.Kodi kapena iwo asankha kuti aziwapembedza atetezi ena m’malo mwake? Koma Mulungu ndiye Mtetezi. Ndipo ndiye amene amapereka moyo kwa akufa ndipo Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
10.Ndipo pa chilichonse chimene mumatsutsana, chiweruzo chake chili ndiMulunguMwiniwake.AmeneyondiMulunguweniweni, Ambuye wanga ndipo mwa Iye ine ndimakhulupirira ndipo kwa Iye ndiko ndimalapa machimo anga
11.Namalenga wakumwamba ndi dziko lapansi. Iye adalenga anzanu kuchokera pakati panu ndi anzawo kuchokera ku nyama. Mwanjira imeneyi Iye amakulengani inu. Palibe chilichonse chofanana naye ndipo Iye ndi wakumva ndi woona
12.Iye ndiye amene ali ndi makiyi a kumwamba ndi a pa dziko lapansi. Iye amachulukitsa kapena kuchepetsa chakudya cha aliyense amene wamufuna. Ndithudi Iye amadziwa bwino za chinthu china chilichonse
13.Iye wakukhazikitsirani chipembedzo chimene adakhazikitsira Nowa kuti atsatire, ndi chimene tavumbulutsa kwa iwe, ndi chimene tidakhazikitsira Abrahamu ndi Mose ndi Yesu powauza kuti inu mukhazikitse chipembedzo ndipo musapatukane. Ndi kovuta kuti anthu osakhulupirira atsatire zimene iwe uwaitanira. Mulungu amasankha yekha onse amene wawafuna ndipo amatsogolera onse amene amagonja kwa Iye
14.Koma iwo adapatukana pamene nzeru zidadza kwa iwo ndipo anali kuchitirana mwano. Koma kukadakhala kuti padalibe mawu amene adanenedwa kale kuchokera kwa Ambuye wako wokhudza chimaliziro, chiweruzo chikadadza kale pa iwo. Ndipo, ndithudi, iwo amene adalandira Buku pambuyo pawo, ndithudi, ali ndi chikayiko chachikulu pa icho
15.Kotero pitiriza kuwaitana ndipo limbikira potsatira njira yoyenera monga momwe walamulidwira. Iwe usatsatire zilakolako zawo zachabe, ndipo nena, “Ine ndimakhulupirira mawu onse a Mulungu amene wavumbulutsa mu Buku lake, ndipo ine ndalamulidwa kuonetsa chilungamo pakati panu. Mulungu ndi Ambuye wathu ndiponso Ambuye wanu. Kwa ife ntchito zathu ndipo kwa inu ntchito. Ndipo palibe mkangano pakati pa ife ndi inu. Mulungu adzatisonkhanitsa tonse ndipo ndi kwa Iye kumene tonse tidzabwerera.”
16.Ndipo iwo amene amatsutsa za Mulungu atavomereza kale kuti adzamumvera, mitsutso yawo siidzakhala yomveka kwa Ambuye wawo ndipo mkwiyo wake udzadza pa iwo ndipo iwo adzalangidwa kwambiri
17.Ndi Mulungu amene watumiza Buku mwachoonadi ndi muyeso. Kodi ndi chiyani chimene chingakudziwitseni inu kuti mwina ola lachiweruzo lili pafupi
18.okhawo amene sakhulupilira amafuna kuti ola lidze msanga pamene onse amene amakhulupirira amaliopa ilo chifukwa amadziwa kuti ndi loonadi. Ndithudi onse amene amakana za olali ndi otayika kwambiri
19.Mulungu ndi wachifundo ndi wachisoni kwa akapolo ake. Iye amapereka chakudya kwa aliyense amene wamufuna. Ndipo Iye ndi wamphamvu ndi Mwini mphamvu zonse
20.Aliyense amene afuna zabwino za m’moyo umene uli nkudza, Ife tidzamupatsa zambiri ndipo wina aliyense amene afuna zabwino za m’moyo uno tidzamupatsa koma iye sadzakhala ndi gawo lina m’moyo umene uli nkudza
21.Kodi kapena iwo ali ndi anzawo amene akhazikitsa chipembedzo china popanda chilolezo cha Mulungu? Ndipo pakadapanda kuti mawu adanenedwa kale, chiweruzo chikadafika kale pakati pawo. Ndithudi anthu ochita zoipa adzalandira chilango chowawa kwambiri
22.Iwe udzawaona anthu ochimwa ali ndi mantha chifukwa cha ntchito zawo ndipo ndithudi mazunzo adzadza pa iwo pamene iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, adzakhala ku Paradiso. Iwo adzalandira, kuchokera kwa Ambuye wawo zonse zimene adzafuna. Chimenechi ndicho chisomo chachikulu
23.Imeneyi ndi nkhani yabwino imene Mulungu ali kuwauza akapolo ake amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino. Nena, “Ine sindili kukupemphani malipiro ayi kupatula kuti muzionetsa chikondi kwa ine chifukwa cha ubale wanga ndi inu.” Ndipo aliyense amene alandira chabwino, tidzamuonjezera zabwino zambiri mofanana ndi izo. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wokonzeka kulipira
24.Kapena iwo akuti, “Iye wapeka yekha bodza lokhudza Mulungu?” Ngati Mulungu akadafuna akadatseka mtima wako. Ndipo Mulungu amafafaniza bodza ndi kukhazikitsa choonadi ndi mawu ake. Ndithudi Iye amadziwa zinsinsi zonse zimene zili m’mtima
25.Ndiye amene amavomera kulapa kwa akapolo ake ndipo Iye amawakhululukira machimo awo ndipo Iye amadziwa zonse zimene mumachita
26.Ndipo Iye amayankha onse amene amakukhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino ndipo amawapatsa zambiri kuchokera ku chisomo chake. Akakhala anthu osakhulupirira iwo adzalandira chilango chowawa
27.Ndipo ngati Mulungu akadaonjezera zabwino kwa akapolo ake, ndithudi, iwo akadaswa malamulo mopyola muyeso pa dziko lonse. Koma Iye amatumiza atayesa mwachifuniro chake. Ndithudi Iye amalemekeza akapolo ake, amadziwa zonse ndipo amayang’anitsitsa akapolo ake
28.Ndipo ndiye amene amagwetsa mvula pa nthawi imene iwo ataya chikhulupiriro ndipo amaonetsa chifundo chake ponseponse. Ndipo Iye ndiye Mtetezi wamphamvu ndi Woyenera kulemekezeka
29.Ndipo pakati pa zizindikiro zake, pali kalengedwe ka kumwamba ndi dziko lapansi ndi zolengedwa zamoyo zimene adazimwaza monsemu. Ndipo Iye ali ndi mphamvu yozisonkhanitsa zonse pamodzi pamene Iye wafuna
30.Ndipo mavuto onse amene amagwa pa inu amadza chifukwa cha ntchito zanu. Komabe Iye amakukhululukirani zolakwa zanu zambiri
31.Ndipo inu simungathe kuthawa padziko lapansi ndipo inu mulibe wina aliyense kupatula Mulungu amene angakutetezeni kapena kukuthandizani
33.Ngati Iye afuna, Iye amaimitsamphepondipoiwoamaimaosayendapamwamba pa nyanja. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa aliyense amene amapirira ndipo amayamika
34.Kapena akhoza kuwaononga chifukwa cha zolakwa zimene iwo adachita. Koma Iye amawakhululukira zolakwa zambiri
36.Motero chilichonse chimene mwapatsidwa padziko lapansindichongosangalatsacham’moyounokomachimene chilindi Mulungundichabwinondiponsochosathakwaiwo amene amakhulupirira ndipo amaika chikhulupiriro chawo mwa Ambuye wawo
37.Ndi iwo amene amapewa kuchita machimo aakuluakulu ndi zinthu zochititsa manyazi ndipo pamene akwiya amakhululuka
38.Iwo amene amamvera kuitana kwa Ambuye wawo ndipo amapemphera panthawi yake amachita zinthu zawo atakambirana ndiponso amapereka kuchokera ku zinthu zimene tawapatsa iwo
40.Ndipo kubwezera kwa ntchito zoipa ndi choipa cholingana ndi ntchitozo ngati munthu akhululukira mnzake ndi kusintha maganizo ake, iye adzalandira mphotho yake kuchokera kwa Mulungu. Ndithudi Iye sakonda anthu osalungama
42.Mlandu uli pa iwo amene amapondereza anthu pochita zoipa ndipo mwamwano amaswa malamulo mopyola muyeso padziko. Ndipo kwa otere kudzakhala chilango chowawa kwambiri
43.Ndipo, ndithudi, aliyense amene aonetsa kupirira ndi chikhululukiro, chimenechi ndi chimodzi cha zinthu zimene zimayamikidwa ndi Mulungu
44.Kwa aliyense amene Mulungu amusocheretsa, kulibe wina amene angamuteteze. Ndipo iwe udzawaona anthu ochita zoipa pamene iwo adzaona chilango ali kunena kuti, “Kodi pali njira yoti tingathe kubwerera?”
45.Ndipo iwe udzawaona ali kubweretsedwa kuchilango monyozedwa ndipo ali ndi nkhope zachisoni. Ndipo iwo amene amakhulupirira adzati, “Ndithudi otayika ndi anthu amene adzitaya ndi owatsatira awo patsiku lachiweruzo. Ndithudi anthu ochita zoipa adzakhala ku chilango chosatha.”
46.Ndipo iwo sadzakhala ndi abwenzi oti awathandize kupatula Mulungu. Ndipo aliyense amene Mulungu wamusocheza alibe wina womutsogolera
47.Kotero bwererani kwa Ambuye wanu mwamsanga tsiku limene simungathe kubwerera lisanadze. Inu simudzakhala ndi kothawira pa tsiku limeneli ndipo inu simudzakhala ndi mwayi wokana
48.Koma ngati iwo akana, Ife sitidakutumize iwe ngati owayang’anira iwo. Udindo wako ndi kungopereka uthenga. Ndipo, ndithudi, ngati Ife timupanga munthu kulawa chisomo chathu, iye amasangalala kwambiri chifukwa cha chisomocho koma ngati vuto lidza pa iwo chifukwa cha zolakwa zawo zimene adachita, ndithudi munthu amakhala osayamika
49.Ufumu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi Mwini wake ndi Mulungu. Ndipo Iye amalenga chimene wafuna. Iye amapereka ana aakazi kwa amene Iye wamufuna ndipo amapereka ana aamuna kwa amene wamufuna
50.Kapena amawapatsa, ana aamuna ndi ana aakazi, ndipo amapanga amene wamufuna kuti akhale chumba. Ndithudi iye amadziwa zonse ndipo amatha kuchita chilichonse
51.Si koyenera kuti Mulungu ayankhule ndi munthu kupatula kudzera m’chivumbulutso kapena kuchokera kumalo obisika kapena potumiza Mtumwi kudzawauza, chimene Mulungu afuna ndi chilolezo chake. Ndithudi Iye ndi wapamwamba ndi wanzeru zosatha
52.Kotero, mwaulamuliro wathu, tatumiza chivumbulutso chathu kwa iwe. Iwe siumadziwa kuti chivumbulutso chidali chiyani kapena kuti chikhulupiriro chidali chiyani. Koma Ife tachipanga icho kukhala muuni umene timatsogolera nawo akapolo athu mwachifuniro chathu. Ndithudi iwe umalangiza anthu ku njira yoyenera
53.Njira ya Mulungu amene ali Mwini wake wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndi chilichonse chimene chili pa dziko lapansi. Ndithudi kwa Mulungu zinthu zonse zimabwerera