4.M’zaka zowerengeka. Mulungu ndiye Mwini ulamuliro ndipo pa tsiku limeneli onse okhulupirira adzakondwera
5.Ndi chithandizo cha Mulungu. Iye amathandiza aliyense amene wamufuna. Iye ndi wamphamvu, ndiponso Mwini chisoni chosatha
7.Iwo amangodziwa zokhazo zimene amaziona za m’moyo uno koma za m’moyo umene uli nkudza, iwo safuna kumva china chilichonse cha izo
8.Kodi iwo saganizira pa okha kuti Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zinthu zonse zimene zikhala m’menemo mwachoonadi ndi mwa kanthawi yokhazikitsidwa? Ndipo, ndithudi, anthu ambiri amakana zoti adzakumana ndi Ambuye wawo
9.Kodi iwo sadayende pa dziko ndi kuona zimene zidawaonekera anthu amene adalipo kale? Iwo adali ndi mphamvu zambiri kuposa awa, ndipo adakumba nthaka ndiponso adamanga pa nthakayo nyumba zambiri kuposa zimene awa amanga. Ndipo kudadza kwa iwo Atumwi awo ndi chiphunzitso chomveka ndipo sikudali koyenera kuti Mulungu awachitire zinthu zosalungama koma kuti iwo adalakwira mizimu yawo
10.Choipa chidatsata munthu amene anali kuchita zoipa chifukwa iwo adakana chiphunzitso cha Mulungu ndipo anali kuwaseka iwo
13.Ndipo iwo sadzakhala ndi ena alionse owathandiza ochokera pakati pa milungu yawo imene anali kupembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo iwo adzakhala okana milungu yawo
15.Ndipo onse amene adakhulupirira ndipo adachita ntchito zabwino, iwo adzasangalatsidwa m’munda wa Paradiso
16.Iwo amene sadakhulupirire ndipo adakana chiphunzitso chathu ndi kukumana kwa m’moyo umene uli nkudza, awa ndiwo amene adzatengedwa kupita ku chilango
18.Inde. Kwa Iye kukhale kuyamikidwa kumwamba ndi padziko lapansi ndiponso pa nthawi yamasana ndi yamadzulo
19.Iye ndiye amene amadzutsa anthu kuchokera ku anthu akufa ndipo amadzutsa anthu akufa kuchokera ku anthu amoyo ndiponso amapereka moyo ku nthaka ikafa. Ndipo mmenemo ndi mmene mudzaukitsidwire
20.Ndipo chimodzi cha zizindikiro zake ndi chakuti Iye adakulengani inu kuchokera ku fumbi, ndipo inu, ndinudi, anthu amene mudamwazidwa
21.Ndipo pakati pa zizindikiro china ndi chakuti Iye adalenga akazi kuchokera mwa inu kuti mukhoza kupeza mpumulo mwa iwo ndipo adaika pakati panu chikondi ndi chisoni. Ndithudi muli phunziro muichi kwa anthu amene amaganiza bwino
22.Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi kalengedwe ka kumwamba ndi dziko lapansi ndi kusiyana kwa zilankhulo zanu ndiponso maonekedwe a makungu anu. Ndithudi mu chimenechimulizizindikirokwaanthuophunzira
23.Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi kugona kumene mumagona usiku ndi usana kufunafuna chisomo chake. Ndithudi mu chimenechi muli chizindikiro kwa anthu amene amatha kumva
24.Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi chakuti Iye amakuonetsani mphezi imene imakuchititsani mantha ndiponso kukupatsani chikhulupiriro. Ndipo amatumiza mvula kuchokera ku mitambo ndiponso amapereka moyo ku nthaka ikafa. Ndithudi mu chimenechi muli zizndikiro kwa anthu ozindikira
25.Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi chakuti kumwamba ndi dziko lapansi zimadzichepetsa potsatira malamulo ake ndipo pamene Iye akuitanani inu kamodzi kokha kuchokera m’nthaka, Taonani inu mudzadza mwamsanga msanga
26.Ndipo chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi ndi chake ndipo zonse zimamumvera Iye
27.Ndipo Iye ndiye amene amayambitsa chilengedwe ndipo adzachibwerezanso ndipo zimenezi ndi zapafupi kwa Iye. Ndipo wake ndi ulemerero kumwamba ndi padziko lapansi. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse
28.Iye ali kupereka chitsanzo chokhudza inu nomwe. Kodi inu muli nawo akapolo amene amakhala anzanu pa zinthu zimene takupatsani ndipo kuti mumagawana nawo zinthuzo mofanana ndiponso mumawaopa iwo monga momwe mumaoperana? Mmenemo ndi mmene timasiyanitsira chiphunzitso chathu kwa anthu amene amazindikira
29.Iyayi! onse osalungama amatsatira zilakolako zawo mosadziwa. Kotero ndani angatsogolere iye amene Mulungu wamusocheretsa? Ndipo iwo sadzakhala ndi wowathandiza
30.Kotero dzipereke kwathunthu ku chipembedzo choonadi, chipembedzo, chenicheni, chimene Mulungu adalamula kuti munthu ayenera kutsatira. Chilengedwe chimene Mulungu adalenga mtundu wa anthu sichingasinthidwe. Ndithudi pali Mulungu, icho ndicho chipembedzo choona. Koma ambiri a mtundu wa anthu sadziwa
31.Lapani kwa Iye ndiponso muopeni Iye. Pitirizani kupemphera nthawi zonse ndipo musakhale inu pakati pa iwo amene amafanizira milungu ina ndi Mulungu weniweni
32.Pali anthu amene amagawa chipembedzo chawo ndi kukhala mipingo yosiyanasiyana ndipo mpingo uliwonse umasangalala ndi zimene uli nazo
33.Ndipo pamene mavuto adza pa anthu, iwo amalira kwa Ambuye wawo ndi kudza kwa Iye modzichepetsa. Koma pamene Mulungu awaonetsa gawo lachisoni chochokera kwa Iye Mwini, ena a iwo amayamba kupembedza milungu ina yoonjezera pa Ambuye wawo
34.Akhala ngati ali kuonetsakusathokozapazimenetawachitira. Basangalalani mwa kanthawi kochepa ndipo posachedwapa mudzadziwa kupusa kwanu
35.Kodi kapena Ife tidawatumizira lamulo limene limanena za zinthu zimene iwo amazipembedza zoonjezera pa Mulungu
36.Ndipo pamene tiwaonetsera anthu chifundo chathu, iwo amasangalala kwambiri chifukwa cha chifundocho ndipo ngati choipa chidza pa iwo chifukwa cha zimene iwo achita ndi manja awo, taonani! Iwo amadandaula kwambiri
37.Kodi iwo saona kuti Mulungu amapereka moolowa manja kwa aliyense amene Iye wamufuna ndiponso zomupatsazochepa munthu yemwe wamufuna. Ndithudi mu chimenechi muli phunziro kwa anthu okhulupirira
38.Kotero apatseni zosowa zawo abale anu, anthu osauka ndi a paulendo. Ichi ndicho chinthu chabwino kwambiri kwa iwo amene afuna chisangalalo cha Mulungu ndipo awa ndiwo amene ali opambana
39.Chimene mumapereka ngati chiongoladzanja kuti chionjezere chuma cha anthu, sichidzakhala ndi chionjezero kwa Mulungu. Koma zopereka zimene mupereka ngati chaulere ndi cholinga chopeza madalitso a Mulungu ndi chimenechi chimene chidzaonjezeredwa kwambirimbiri
40.Ndi Mulungu amene anakulengani inu amene amakupatsani zofuna zanu. Iye adzakonza kuti mufe patsogolopakepanondipokenakaadzakupatsaninsomoyo. Kodi chilipo china chilichonse chimene mungachifanizire ndi chimene chingachite zimenezi? Ulemerero ukhale kwa Iye ndipo Iye akhale zopambana kuposa zonse zimene amazifanizira ndi Iye
41.Zinthu zoipa zalowa m’dziko ndiponso m’nyanja chifukwa cha ntchito za anthu zimene amachita ndi manja awo. Mulungu akhoza kuwalawitsa chilango chifukwa cha ntchito zawo kuti mwina athe kutembenuka
42.Nena “Pitani paliponse pa dziko ndi kuona zimene zidawaonekera anthu amene adalipo kale. Ambiri a iwo adali opembedza mafano.”
43.Kotero dziperekeni kwathunthu ku chipembedzo choona lisanadze tsiku loopsa kuchokera kwa Mulungu limene silidzatheka kulizemba. Pa tsiku limeneli anthu adzagawidwa m’magulu
44.onse osakhulupirira adzalangidwa chifukwa cha kusakhulupirira kwawo ndipo onse amene amachita ntchito zabwino adzadzisungira zinthu zabwino kumwamba
45.Ndipo Iye adzawapatsa malipiro abwino onse amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino kuchokera ku zokoma zake. Ndipo Iye sakonda anthu osakhulupirira
46.Ndipo chimodzi mwa zizindikiro zake ndi chakuti amatumiza mphepo imene imabweretsa zabwino ndi cholinga choti mulawe chisomo chake ndiponso kuti zombo ziyende mwamalamulo ake ndiponso kuti inu muzifunafuna chifundo chake ndi kumuthokoza
47.Ndithudi Ife tidatumiza, Atumwi kwa anthu awo iwe usanabadwe ndipo iwo adadza kwa iwo ndi chiphunzitso choyenera. Ife tidapereka chilango kwa anthu ochimwa ndipo kuthandiza anthu okhulupirira ndi udindo wosatha kwa Ife
48.Mulungu ndiye amene amatumiza mphepo kuti iyendetse mtambo ndipo amaumwaza mlengalenga monga momwe wafunira. Iye amauphwanya ndipo inu mumaona mvula ili kugwa kuchokera mu mtambowo. Iye amagwetsa mvula pa akapolo ake amene wawafuna. Taonani! Iwo amakhala osangalala
50.Taonani zizindikiro za chisoni cha Mulungu mmene amaperekera moyo ku nthaka imene inali yakufa. Ndithudi Iye adzadzutsa zakufa kuti zikhale zamoyo. Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
51.Ndipo ngati Ife tikatumiza mphepo imene imapangitsa mbewu zawo kusanduka za chikasu, iwo amakhala osathokoza
52.Ndithudi iwe siungathe kumupanga munthu wakufa kuti amve ndiponso siungathe kumupanga munthu wosamva kuti amve kuitana pamene iwo atembenuka ndi kuthawa
53.Ndipo iwe siungathe kumutsogolera munthu wakhungu kuti asiye kulakwa kwake. Palibe amene adzakumvera kupatula okhawo amene amakhulupirira mu chiphunzitso chathu
54.di Mulungu amene adakulengani inu ofoka ndipo adakupatsani mphamvu pambuyo pa kufoka. Ndipo atakupatsani mphamvu adakupatsani kufoka ndi imvi. Iye amalenga chilichonse chimene wafuna ndipo ndiye amene amadziwa zonse ndipo ndiye Mwini mphamvu
55.Ndipo pamene ola lidzadza, anthu ochimwa adzalumbira kuti adangokhala ola limodzi lokha. Kotero iwo amakhala onamizidwa
56.Ndipo iwo amene adapatsidwa nzeru ndi chikhulupiriro adzati, “Ndithudi inu mwakhala molingana ndi malamulo a Mulungu mpaka pa tsiku louka kwa akufa. Kotero ili ndilo tsiku louka kwa akufa koma inu simunalidziwe ayi.”
58.Ndithudi m’Buku ili la Korani anthu tawaikiramo zitsanzo zambiri zosiyanasiyana ndipo ngati iwe utawabweretsera chiphunzitso iwo amene sakhulupirira adzati, “Iwe siuli kutsatira china chilichonse koma bodza ndi matsenga.”
60.Kotero pirirani. Lonjezo la Mulungu ndi loona ndipo usalole anthu opanda chikhulupiriro kuti akuderere iwe