3.Amene amapitiriza kupemphera ndipo amapereka msonkho wothandiza anthu osauka ndiponso amakhulupirira kwambiri m’moyo umene uli nkudza
4.Ndithudi iwo ndi amene amakana za moyo umene uli nkudza. Ife tazipanga ntchito zawo kuti zioneke ngati zabwino motero iwo amayenda mwakhungu
7.Pamenepo Mose adauza banja lake kuti, “Ine ndili kuona moto. Ine posachedwapa ndikubweretserani nkhani kapena khala la moto kuti mukhoza kuotha.”
8.Ndipo pamene iye adafika pamoto paja, mawu adamveka akunena naye kuti, “odalitsidwa ndiye amene ali mu moto uwu ndiponso alionse a pamalo pozungulira. Ulemerero ukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwe zonse.”
10.“Ponya ndodo yako pansi.” Ndipo pamene iye adaona kuti ilikuyenda ngati njoka, adatembenuka ndi kuthawa ndipo sadayang’ane m’mbuyo. “Iwe Mose!” Atumwi anga sachita mantha pamene ali ndi Ine
11.Akakhala iwo amene amalakwa ndipo amachita zabwino pambuyo pochita zoipa Ine ndine wokhululukira ndiponso wachisoni chosatha
12.“Pisa dzanja m’thumba mwako. Litulutse lili loyera ngakhale kuti siudapweteke. Ichi ndi chimodzi cha zizindikiro zisanu ndi zinayi zimene zidzaonetsedwa kwa Farawo ndi anthu ake. Ndithudi iwo ndi anthu ochimwa kwambiri.”
13.Pamene zizindikiro zathu zooneka bwino zinaonetsedwa kwa iwo, iwo adati, “Uwu ndiwo ufiti weniweni.”
14.Mitima yawo idadziwa kuti zizindikiro zidali zoona koma adazikana izo chifukwa chakulakwa ndiponso kunyada kwawo. Taona zimene zidawaonekera anthu olakwa
15.Ndithudi Ife tidapereka nzeru kwa Davide ndi Solomoni. Iwo adati, “Kuyamikidwa ndi kwa Iye amene watikweza ife kukhala pamwamba pa akapolo ake ambiri okhulupirira.”
16.Solomoniadalowam’malomwaDavide.Iye adati, “Oh inu anthu anga! Ife taphunzitsidwa chiyankhulo cha mbalame ndipo tapatsidwa zinthu zabwino zambiri. Ndithudi ichi ndi chifundo choonekeratu.”
17.Asirikali a nkhondo a mtundu wa majini, anthu ena ndi mbalame anasonkhanitsidwa pamaso pa Solomoni ndipo adaimitsidwa pa mizere m’magulu osiyanasiyana mogwirizana ndi maudindo
18.Mpaka pamene iwo anafika pa chigwa cha nyerere, nyerere ina idati, “Oh inu nyerere! Lowani ku maenje anu chifukwa mwina Solomoni pamodzi ndi Asirikali ake, akhoza kukuonongani mosadziwa.”
19.Solomoni adamwetulira posangalatsidwa ndi mawu ake ndipo iye adati, “Ndilangizeni Ambuye kuti ndizikuthokozani pa zabwino zonse zimene mwandipatsa ine ndi makolo anga ndiponso kuti ndizichita ntchito zabwino zimene zimakukondweretsani inu. Ndilowetseni ine ku Paradiso kudzera m’chisomo chanu, kuti ndikhale pakati pa akapolo anu angwiro.”
20.Iye adayendera mbalame nati, “Kodi mbalame yotchedwa mnthengu ili kuti? Kodi kapena iyo ili pamodzi ndi amene sadabwere?”
21.“Ndithudi ndidzailanga iyo ndi chilango chowawa kapena ndidzaipha kupatula ngati ibweretsa kwa ine chifukwa chomveka.”
22.Ndipo mbalame ya mnthengu siidachedwe ndipo idati, “Ndadziwa zimene iwe siudziwa ndipo ndikubweretsera nkhani yoona kuchokera ku Saba.”
23.“Ine ndapeza munthu wamkazi akulamulira iwo ndipo iye wapatsidwa zinthu zonse zomuyenereza ndipo ali ndi Mpando waukulu wachifumu
24.Ndidamupeza iye pamodzi ndi anthu ake ali kupembedza dzuwa moonjezera pa Mulungu ndipo Satana wawakongoletsera ntchito zawo zoipa ndipo wawasocheretsakunjirayoyenerandipoiwosiotsogozedwa bwino.”
25.Ndi kuti sapembedza Mulungu amene amaulula zobisika za kumwamba ndi pa dziko lapansi ndipo Iye amadziwa zimene inu mumabisa ndi zimene mumaulula
30.Kalatayi ndi yochokera kwa Solomoni ndipo ikuti, “M’dzina la Mulungu, Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha.”
32.Iye adati, “oh inu mafumu! Ndipatseni chilangizo chokhudza nkhani iyi ndipo sindilamula china chilichonse pokhapokha inu mutakhalapo.”
33.Iwo adati, “Ife ndife olimba mtima ndiponso odziwa kumenya nkhondo molimba, ndipo nkhani ili kwa iwe. Ndipo udziwe mmene ungalamulire.”
34.Iye adati, “Ndithudi mafumu akalowa mu mzinda amaononga mwaupandu ndi kuwasandutsa anthu olemekezeka kukhala onyozeka. Umo ndi mmene iwo amachitira.”
36.Ndipo pamene akazembe adadza kwa Solomoni, iye adati, “Kodi muli kundipatsa chuma chambiri? Icho chimene Mulungu wandipatsa ine ndi chabwino kuposa chuma chonse chimene wakupatsani inu. Koma inu mumasangalala ndi mphatso zanu.”
37.“Bwererani kwa iwo. Ife tidzapita kwa iwo ndi magulu ankhondo amene iwo sangathe kuwagonjetsa ndipo tidzawathamangitsa m’dziko lawo mochititsa manyazi ndipo iwo adzanyozeka.”
38.Iye adati, “oh inu mafumu! Kodi ndani amene angandibweretsere mpando wake wachifumu iwo asanabwerekwainemogonja?”
39.Winawamphamvu, amene adalimmodziwamajiniadati,“Inendidzakubweretseraniinu musadanyamuke pa mpando wanu. Ine ndili ndi mphamvu zonyamulira mpando ndiponso ndine wokhulupirika.”
40.Koma wina amene anali kudziwa Mawu a Mulungu adati “Ine ndidzakubweretserani msanga musadaphenire maso anu.” Ndipo pamene iye adaona kuti mpando wabwera kwa iye adati, “Ichi ndi chisomo cha Ambuye wanga kuti andiyese ngati ndikuthokoza kapena sindikuthokoza. Ndipo aliyense amene athokoza atero podzipezera yekha zabwino. Ndipo amene sathokoza ndithu, Ambuye wanga ali ndi zonse ndipo ndi Wolemekezeka.”
41.Ndipo iye adati, “Sinthani mpando wake wachifumu kuti tione ngati iye akhoza kuuzindikira kapena ayi.”
42.Ndipo pamene mfumukazi inadza kwa Solomoni idafunsidwa kuti, “Kodi mpando wako wachifumu ndi otere?” Iye adati, “Ukukhala ngati umenewu” ndipo ife tinadziwa kale ndipo tagonja kwa Mulungu mwamtendere.”
43.Zinthu zimene amapembedza zoonjezera pa Mulungu ndi zimene zamusokoneza. Iye adali mmodzi wa anthu osakhulupirira
44.Iye adauzidwa kuti, “Lowa mnyumba yachifumu.” Ndipo pamene iye anaiona iyo, adaganiza kuti ndi dziwe la madzi ndipo miyendo yake adaionetsa poyera. Solomoni adati, “Iyi ndi nyumba yachifumu yomatidwa ndi magalasi.” Iye adati, “Ambuye, ine ndalakwira mzimu wanga. Tsopano ndili kudzipereka pamodzi ndi Solomoni kwa Mulungu, Ambuye wazolengedwa zonse.”
45.A Thamoud, ndithudi, tidawatumizira m’bale wawo Saleh, amene adati, “Muzipembedza Mulungu basi.” Koma iwo adagawikana m’magulu awiri okangana
46.Iye adati, “Anthu anga! Kodi bwanji mufuna kubweretsa choipa msanga musanabweretse chabwino? Nanga ndi chifukwa chiyani simupempha chikhululukiro kwa Mulungu kuti mukhoza kupeza chisomo chake?”
47.Iwo adati, “Ife tili kuona choipa chochokera kwa iwe ndiponso kwa anthu amene amakutsatira iwe.” Iye adati, “Choipa chimene muli kuchiona chili kuchokera kwa Mulungu. Inu ndinu anthu amene muli kuyesedwa.”
48.M’mizinda mwawo mudali anthu asanu ndi anayi amene anali kuchita zoipa mdziko ndipo samachita zabwino ayi
49.Iwo adati, “Tiyeni tonse tilumbire, dzina la Mulungu, kuti timuphe nthawi ya usiku pamodzi ndi a pabanja lake lonse. Ndipo tidzawauza abale ake kuti, “Ife kudalibe pamene iwo anali kuphedwa. Ndipo zimene tili kunena ndi zoona zokhazokha.”
52.Chifukwa chakuti iwo adalakwa, nyumba zawo zimene anali kukhalamo tsopano ndi mabwinja. Ndithudi m’zimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira
55.“Kodi inu muli kuchita chiwerewere ndi amuna anzanu pokwaniritsa zilakolako zanu ndi kusiya akazi? Inu ndinu mbuli basi.”
56.“Yankho lawo silidali lina koma kuti, “Chotsani anthu a Loti mu mzinda wanu. Awa ndi anthu amene afuna kudziyeretsa.”
58.Ndipo tidawalasa iwo ndi mvula ya miyala imene idagwa pa iwo. Ndi mvula yoipa imene idagwera iwo amene adachenjezedwa
59.Nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu ndipo mtendere ukhale pa Atumwi ake amene Iye wawasankha. Kodi wabwino ndani Mulungu kapena mafano amene amawapembedza yoonjezera pa Mulungu?”
60.Kapena wabwino ndi Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi kukutumizirani mvula kuchokera kumwamba ndi kubweretsa minda ya chisangalalo? Iwo sangathe kumeretsa mitengo. Kodi pali milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni? Koma iwo ndi anthu amene amafanizira ena ake kukhala ofanana ndi Mulungu
61.Kapena Iye amene adakhazikitsa dziko ndi kulithirira ilo ndi mitsinje ya madzi oyenda; ndipo wakhazikitsa mapiri pa dziko ndipo waika malire pakati pa nyanja ziwiri. Kodi pali mulungu wina woonjezera pa Mulungu weniweni? Koma ambiri a iwo ndi osadziwa
62.Kapena Iye amene amayankha mapemphero a munthu opanikizika pamene amupempha Iye ndipo amamuchotsera mavuto. Ndiyetu amene wakupatsani dziko lapansi kuti muzikhalamo. Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Ndi zazing’ono zimene mumakumbukira
63.Kapena ndi Iye amene amakutsogolerani mu mdima pa mtunda kapena pa nyanja ndipo amatumiza mphepo ngati yonyamula uthenga wabwino wa chisomo chake. Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Mulungu ndi wapamwamba kuposa zimene amamufanizira nazo
64.Kapena Iye amene poyambirira adapanga zolengedwa ndiponso amene adzatidzutsanso kukhala ndi moyo m’moyo umene uli nkudza ndiponso amene amakupatsani chakudya kuchokera ku nthaka ndi kumwamba? Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Nena, “Tionetseni chizindikiro chanu ngati zimene mukunenazi ndi zoonadi.”
65.Nena, “Palibe amene ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene amadziwa zobisika kupatula Mulungu. Ndiponso anthu sadziwa nthawi imene adzaukitsidwa kukhalanso ndi moyo.”
66.Kodi kuzindikira kwawo m’moyo umene uli nkudza kwakwaniritsidwa? Iwo ndi okaika pa zamoyo umene uli nkudza ndipo maso awo ndi otsekeka pa za iwo
67.Anthu osakhulupirira adati, “Kodi pamene ife ndi makolo anthu, tisanduka dothi tidzaukitsidwanso?”
68.“Ndithudi ife tidalonjezedwa ndiponso makolo athu. Ichi si china ayi koma nkhani zopanda pake za anthu akale.”
71.Ndipo iwo amati, “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati zimene muli kunenazi ndi zoona?”
74.Ndipo, ndithudi, Ambuye wako amadziwa zonse zimene zimabisika m’mitima mwawo ndiponso zonse zimene amaulula
75.Kulibe chinsinsi kumwamba kapena padziko lapansi chimene sichidalembedwe mu Buku lake lolemekezeka
78.Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo ndi chiweruzo chake. Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini kudziwa za chinthu china chilichonse
80.Ndithudi iwe siungathe kumupanga munthu wakufa kuti amve ndiponso siungathe kumupanga munthu osamva kuti amve kuitana kwako pamene iye atembenuka
81.Si udindo wako kutsogolera anthu a khungu kuti aleke kusochera. Palibe munthu amene adzakumvera kupatula okhawo amene amakhulupirira mu chivumbulutso chathu ndipo amadzipereka kwathunthu
82.Patsiku limene chiweruzo chathu chidzayandikira kwa osakhulupirira, Ife tidzawabweretsera chinyama chimene chidzayankhula nawo kuchokera ku dziko lapansi chifukwa munthu sanakhulupirire chivumbulutso chathu
83.Patsiku limeneli, tidzasonkhanitsa kuchokera ku mtundu uliwonse gululaanthuamenesadakhulupirirechivumbulutsochathu. Iwo adzasonkhanitsidwa ndi kuikidwa m’mizere
84.Mpaka pamene adzafike pamalo a chiweruzo, Mulungu adzati, “Kodi inu mudakana chivumbulutso changa ngakhale kuti inu simumadziwa chilichonse cha chivumbulutsocho? Kodi ndi chiyani mumachita?”
86.Kodi iwo saona mmene tidakonzera usiku kuti ukhale mpumulo ndi masana kuti uziwapatsa kuwala? Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira
87.Patsikulimeneli, lipengalidzalizidwandipoonseamene amakhala kumwamba ndi padziko lapansi adzagwidwa ndi mantha kupatula okhawo amene Mulungu adzafuna kuwapatula mu zimene zi. Onse adzabwera kwa Iye modzichepetsa
88.Iwe udzaona mapiri ndi kuwaganizira kuti ndi okhazikika koma iwo adzayenda ngati mmene mitambo imachitira. Uwu ndi mchitidwe wa Mulungu amene wakonza bwino lomwe chinthu chilichonse. Ndithudi Iye amadziwa bwino zonse zomwe mumachita
89.Iwo amene achita zabwino adzalandira mphotho imene ili yabwino ndipo adzakhala osakhudzidwa ndi zochititsa mantha za tsiku limeneli
90.Koma iwo amene achita zoipa adzaduduluzidwa pa mphumi zawo kunka ku moto. “Kodi inu simudzalandira malipiro ofanana ndi ntchito zanu?”
91.Nena, “Ine ndalamulidwa kutumikira Ambuye wa mzinda uno umene waupanga kuti ukhale Woyera. Zinthu zonse ndi zake. Ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi mwa odzipereka.”
92.Ndipo ndalamulidwa kuwerenga Buku la Korani. Aliyense amene atsatira njira yoyenera atero podzithandiza yekha. Kwa iye amene asochera nena “Ine si ndine kanthu kena koma mmodzi wa iwo ochenjeza anthu.”
93.Ndipo nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu! Iye adzakulangizani zizindikiro zake ndipo inu mudzazizindikira. Ambuye wanu saiwala zimene mumachita.”