قاریعہ
الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja
1.
Tsiku louka kwa akufa
2.
Kodi tsiku louka kwa akufa ndi chiyani
3.
Kodi ndi chiyani chimene chidzakuuze iwe kuti tsiku louka kwa akufa ndi chiani
4.
Ndi tsiku limene anthu adzakhala ngati dzombe louluka paliponse
5.
Ndi mapiri adzakhala ngati fumbefumbe za ubweya
6.
Ndipo iye amene muyeso wake wa ntchito zabwino udzakhala wolemera
7.
Adzakhala ndi moyo wa chimwemwe ndi chisangalalo
8.
Koma iye amene muyeso wake wa ntchito zabwino udzapezeka wopepuka
9.
Mudzi wake udzakhala dzenje lamoto
10.
Kodi ndi chiyani chimene chidzakuuze zinthu zonsezi
11.
Ndi moto wa malawi osatha
پچھلی سورہ
اگلی سورہ