٧.Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo, ngati inu nonse mutakhala ndi chikhulupiriro chenicheni
٨.Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Ndipo ndiye amene amapereka moyo ndi imfa. Ambuye wako ndi Ambuye wa makolo ako amene adanka kale
١٧.Ndipo, ndithudi, tidawayesa anthu a Farawo, iwo asanabadwe, ndipo kudadza kwa iwo Mtumwi wolemekezeka
٣٧.Kodi awa ndi opambana kuposa anthu a Tubba ndi iwo amene adalipo kale? Ife tidawaononga onse ndipo iwo adali olakwa
٤٢.Kupatula yekhawo amene waonetsedwa chisomo cha Mulungu. Ndithudi Iye ndiye Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni chosatha
٥٦.Ndipo iwo sadzalawa imfa kupatula imfa yoyamba ndipo Iye adzawapulumutsa ku chilango chowawa cha Gahena
٥٨.Ndithudi Ife taipanga Koraniyi kukhala yapafupi m’chiyankhulo chako ndi cholinga chakuti mwina angathe kukumbukira