٣.Alekeni kuti adye, ndi kuti asangalale ndipo alekeni kuti atangwanike ndi chikhulupiriro chabodza. Iwo adzadziwa posachedwapa
١٦.Ndithudi Ife taika nyenyezi zikuluzikulu kumwamba ndipo tazikongoletsa kuti zizikondweretsa anthu oyang’ana
١٩.Ife tidatambasula dziko lapansi ndi kuikamo mapiri ndipo tameletsa mu ilo zinthu zosiyanasiyana chilichonse chili ndi muyeso wake
٢٠.Ndipo takupatsani mu ilo njira zopezela chakudya chanu ndi cha izo zimene inu simungathe kuzidyetsa
٢١.Palibe chilichonse, chimene nkhokwe yake siili ndi Ife ndipo sititumiza kupatula m’muyeso wodziwika
٢٢.Ndipo Ife timatumiza mphepo yobereketsa ndipo timatsitsa madzi kuchokera kumwamba ndipo timakupatsani kuti mumwe; ndipo inu si ndinu osunga nkhokwe zake
٢٤.Ndipo, ndithudi, Ife timadziwa onse amene adalipo kale inu musanadze ndipo timadziwa mibadwo yanu yatsopano ndi iwo amene adzadza m’tsogolo
٢٥.Ndipo, ndithudi, Ambuye wako adzasonkhanitsa onse pamodzi. Zoonadi Iye ndi Wanzeru ndi Wodziwa chilichonse
٢٦.Ndipo, ndithudi, Ife tidamulenga munthu kuchokera ku dothi lotulutsa mawu, losinthidwa m’matope akuda osalala
٢٨.Ndipo pamene Ambuye wako adati kwa angelo, “Ine ndilenga munthu kuchokera ku dothi lotulutsa mawu losinthidwa matope akuda osalala.”
٢٩.“Motero ndikatha kumukonza ndi kuuzira mpweya umene ndidalenga chifukwa cha iye ndipo nonse gwadani kumulambira iye.”
٣٣.Satana adati, “Ine sindingagwadire munthu amene Inu mwamulenga kuchokera ku dothi lotulutsa mawu losinthidwa matope akuda osalala.”
٣٩.Satana adati, “Oh Ambuye wanga! Popeza Inuyo mwandisocheretsa ine, ndithudi, ndidzawasalalitsira njira yautchimo anthu onse padziko lapansi, ndithudi onse ndidzawasocheretsa
٤٢.“Ndithudi iwe siudzakhala ndi mphamvu pa akapolo anga, kupatula anthu ochita zoipa amene amakutsatira iweyo.”
٤٤.“Iyo ili ndi makomo asanu ndi awiri, ndipo chipata chilichonse chidzakhala ndi anthu ake olowapo.”
٤٧.“Ndipo Ife tidzachotsa m’mitima yawo mkwiyo uliwonse kuti akhoza kukhala pachibale ndi kupumula m’mipando yawofowofo moyang’anizana.”
٥٢.Pamene iwo adadza kwa iye ndi kumuuza kuti, “Mtendere ukhale kwa iwe.’ Koma iye adawayankha kuti, “Ndili ndi mantha ndi inu.”
٥٣.Iwo adati, “Usaope! Ife tadza kwa iwe ndi nkhani yabwino ya mwana wamwamuna amene adzakhala wodziwa zambiri.”
٥٤.Iye adati, “Kodi inu muli kudzandiuza nkhani yabwino pamene ine nditakalamba kale? “Kodi nkhani yanu ndi yotani?”
٦٠.“Kupatula mkazi wake amene ife talamulidwa kuti akhalire m’mbuyo pamodzi ndi iwo amene anali kukhalira m’mbuyo.”
٦٥.“Motero choka ndi abale ako pakati pa usiku, iwe uziyenda pambuyo pawo ndipo usalole wina aliyense kuti atembenuke. Kapita kumene walamulidwa kupita.”
٧٤.Ndipo Ife tidaononga (mizinda yawo) zapansi kukhala pamwamba ndipo tidawagwetsera mvula ya miyala ya moto
٨٥.Ndipo Ife sitidalenge kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo kupatula ndi choonadi. Ndithudi popanda chikayiko tsiku lachiweruzo lidzadza; kotero akhululukireni, kukhululuka kwabwino
٨٧.Ndipo, ndithudi, Ife tidakupatsa mavesi asanu ndi awiri amene amanenedwa kawirikawiri ndi Korani yolemekezeka
٨٨.Usamayang’ane mwanjiru zinthu zokoma zimene tawapatsa ena a iwo kapena kumamva chisoni pa izo. Ndipo onetsani chifundo kwa anthu okhulupirira