الحاج يوسف محمد كنيمولا · chiCheŵa, chinyanja

١.Alif Lam Mim Raa. Awa ndi mavesi a Buku. Chimene chavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako ndi choonadi. Koma anthu ambiri sakhulupirira
١٦.Nena, “Kodi Ambuye wakumwamba ndi pa dziko lapansi ndani?” Nena, “Mulungu.” Nena, “Kodi inu mwasankha milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni imene, ngakhale kwa iyo yokha, singathe kuchita zinthu zoipa kapena zabwino?” Nena, “Kodi anthu a khungu ndi anthu oona ndi ofanana? Kapena mdima umafanana ndi kuwala? Kodi iwo akuphatikiza Mulungu ndi mafano awo? Kodi mafano awo adalenga zinthu zofanana ndi zimene Iye adalenga; kotero kuti zolengedwa zonse zimaoneka kwa iwo ngati zofanana?” Nena, “Mulungu ndi Namalenga wa zinthu zonse. Iye ndi Mmodzi yekha ndipo ndi Mwini Mphamvu zonse.”
٣٣.Kodi Iye amene amayang’anira mizimu yonse ndi ntchito zonse zimene imachita angafanane ndi wina wosadziwa? Komabe iwo amakhazikitsa milungu ina m’malo mwa Mulungu weniweni. Nena, “Itchuleni! Kodi inu mungamuuze Mulungu zinthu zimene Iye sadziwa pa dziko kapena iwo ndi mawu abodza chabe?” Iyayi. Kwa iwo amene sakhulupirira, chiwembu chawo chimaoneka chabwino ndipo iwo atsekerezedwa kutsatira njira yoyenera ndipo aliyense amene Mulungu amamusocheza, kwa iye kulibe amene angamutsogolere